Sermons

Tapulumutsidwa Kuti Tikatumikire Ena

      

Mabuku Owerengedwa: Masalimo 91:1-11, Estere 4:7-17, 1 Akorinto 12:12-20


Mawu Oyamba


Ife Akhrstu ndife anthu opulupumitsidwa chifukwa cha Yesu Khristu. Kubadwa kwake kwa Yesu Khristu ndiko chiyambi cha chipulumutso chathu. Chipulumutso chimenechi chimafika pachimake pamene Yesu anapachikidwa pamtanda nafa, imfa yomwe timakumbukira panyengo ya Pasaka. Chipulumutso chathu chomwe tinachilandira chikuyenera kusefukira kwa anthu ena. Munthu ukapulumuka ku zoopsa monga zachifwamba umafotokozera ena ndipo umafuna kuwachenjeza kuti nawo asamale. Munthu amene waona chisomo cha Mulungu amafuna awagawirenso ena. Pamene tapulumutsidwa timasanduka mfulu ndipo timafuna ena akhalenso mfulu ndipo timayamika Mulungu potichotsa mu nyengo zoopsa. Ndi chifukwa chake ku Masalimo 116:12 Davide akuyamika Mulungu “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” Tionetsere kuthokoza kwathu pamene tikutumkira ena. Tikapumulumutsidwa tiyeni tiganizirenso ndi kupulumutsa komanso kutumikira ena.


Kutambasula Mawu


Mutu umene mpingo wa Zomba ukhale ukulingalira chaka chino ndi Tapulumutsidwa Kuti Tikatumire Ena ndipo mutu wake waung’ono ndi “Kupulumutsidwa mu Nyengo Ino Kuti Titumikire Ena”. Kodi Mulungu akufuna kuti tichite chiyani? Ndi mphatso ziti zimene tingazigwiritse ntchito pa mpingo uno? Tawerenga nkhani ya Estere amene anapatsidwa mwayi wokhala kunyumba yachifumu. Pokhala m’nyumba yachifumu iye anali ndi mphamvu komanso kuthekera kothandiza ndi kutumikira ena. Nthawi zina Mulungu amagwira ntchito mwa ife mwapansipansi. Tsiku likakwana Mulungu amavumbulutsa mphatso zathu.


Mu nkhani ya Estere tikuona Modekai akuchenjeza Estere kuti asakhale chete pamene ayuda ena akuvutika chifukwa akhala chete thandizo litha kuchokera kwina. Estere sanadziwe kuti Mulungu anamuyika m’nyumba yachifumu pofuna kumugwiritsa ntchito mu nyengo yovuta. Kodi ifeyo ndi nkhani ziti zimene tikuyenera kuchitapo kanthu? Ife tikuyenera kutumikira ena chifukwa tapulumutsidwa. Mulungu ali nafe cholinga. Pamene talowa chaka china tipemphe Mulungu atitume kuti tikatumikire ena. Mulungu watisankha chifukwa cha nyengo imene tili nayo. Estere atamva zomwe Modekai anamuyankhula anachita mantha ndjpo anazindikira kuti akuyenera kuchitapo kanthu. Iye monga Myuda anali m’nyumba yachifumu ndi cholinga. Choncho anagwada pansi pa phulusa napempha Mulungu kuti amutume. Anadzichepetsa pamaso pa Mulungu. Nafenso tidzichepetse ndi kumupempha Mulungu kuti atitume. Tidzikhuthule pamaso pa Mulungu kuti achite nafe, timutumikire. Tikonde anthu ena ngati ana a Mulungu. Tikatero titha kuwatumikira. Tiwakonde kuti nawo abowoleze pa zosowa zawo, aone kukoma kwa Mulungu. Tiwaonetsere zomwe Mulungu amachita ndi ife.


Estere akugonjetsa tchimo. Nafenso titero. Hamani anaphedwa pa mtanda umene anakonza kuti apherepo ena - atafa iye, Ayuda onse anapulumuka. Tikachotsa tchimo chikondi cha Mulungu chimaonekera.


Chifukwa chiyani chipulumutso chathu chipulumutse anthu ena? Tawerenga 1 Akorinto 12:12-20 komwe akutiphunzitsa kuti ndife thupi limodzi la khristu- ziwalo zosiyanasiyana. Mulungu watipatsa ntchito komanso mphatso zosiyanasiyana. Ena amatumikira poyendera anzawo, ena amatumikira ndi chuma chawo. Tikuyenera kukhudzidwa ndi nyengo za anzathu ena. Tikazindikira kuti iwonso ndi chiwalo cha Khristu tidzatha kuwafikira ndi kuwatumikira. Ngati Zomba CCAP tikukhudzidwa bwanji ndi nkhanza za amayi ndi ana m’dziko muno? Tikukhudzidwa bwanji ndi mchitidwe wodzimangirira womwe wachuluka? Ngati Zomba CCAP zosowa zathu ndi chiyani? Tichita chiyani kuti tithetse zosowa zathu?


Mawu Otsiriza


Mulungu watisintha kuti tisinthe miyoyo ya anthu ena. Sanatipulumutse kuti tikatumikiridwe. Ambiri timaona mphatso zimene zili mwa ena osati zomwe zili mwa ife. Choncho amafuna anthu ena ndi amene azitumikira. Tiyeni tidzipereke. Kutumikira sikukhala ndi zinthu zambiri. Zochepa zomwezo titha kutumikira nazo ena. Mulungu anamuuza Estere kuti anali m’nyumba yachifumu mu nyengo imeneyo ndi cholinga chakuti atumikire ena. Ifenso tili munyengo iyi kuti tionetse kupulumutsidwa kwathu. Mulungu watiyitana, watipulumutsa kuti tikatumikire ena. Ndife ana ndi antchito a Mulungu. Taomboledwa kudzera mwa mwazi wa mwana wake Yesu. Kuchokera mwa ife anthu ena apeze kubowoleza kwawo, akaone Mulungu akuchita nawo, aone Mulungu akusuntha mpingo wa Zomba. Mulungu akufuna kuti tichite mowonjezera kuposa m’mene tikuchitira panopa.

About Us

Zomba CCAP congregation, located in Zomba City, the old capital of Malawi, was established in 1898, and currently boasts 1,638 Christians, of which 115 are church elders and 103 church deacons. It has vibrant women and youth ministries, and a management team that co-ordinates the work of eleven committees, among which are the partnership, evangelism and intercessory, and music committee, as well as faith and works committee... Read more

Announcements & Events

Explosion 2023 Posted: 13 Apr, 2023
Zomba CCAP Holy Week Time Table Posted: 3 Apr, 2023

Address

Zomba C.C.A.P.
Chimbiya Road
P.O. Box 355, Zomba
+265 995 089 475

Newsletter