Sermons

The Power Of Christ’s Resurrection And Appearances To Believers

      

Scriptures: Luke 24: 13-35, John 11: 25-26


The story of Christ’s resurrection is a remarkable turn to the Christian faith. It separates Christianity from all beliefs in that God came to meet the needs of the people. As illustrated in Romans 5:8 that while we were yet sinners, Christ died for us. The story from Luke 24:13-26 draws out four lessons for us Christians.



  1. Jesus is a true friend to those who are sad and hopelessJesus joined Cleopas and his friend on their path to Emmaus at a time when they had lost hope pf the messiah due to his death. They had become hopeless that the Messiah had been crucified. Jesus rose from the dead to bring comfort and hope to such people. In the context of Malawi, at present, when people are committing suicide at an alarming rate; due to loss of hope, Jesus is here for them, He loves them while they are still hopeless. He rose from the dead for them, so that he can restore their joy and hope.

  2. The greatest enemy in Christian faith is doubtCleopas and his friend were sad and hopeless because they had doubt.  Even the apostles did not believe what Moses had written about the Lord Jesus Christ; that he would rise again. Christ had to remind them of this.Doubt produces sadness, hopelessness in faith and it makes us foolish. Doubting does not please God, for it is a lack of faith and without faith no one can please God.  1 Corinthians 1:18 says, the message of the cross is foolishness to those who are perishing or in doubt but to us, it is the power of God.

  3. God is a God of self-revelationGod is willing to make himself known to his people. Christ revealed himself to Cleopas and his friend and lo their joy was restored. They were excited and they went back to Jerusalem to witness of this. Christ equips believers to be witnesses of the truth through the power of his resurrection. He helps us witness even in the smallest things. Are we witnessing Christ in our work places even in a country where corruption is rampant?As believers we have been called to witness in our lifestyle, not everyone is meant to be a pastor or evangelist but our lives must witness Christ to others.

  4. There is an assurance of life after lifeJohn 11: 25-26Jesus said to her “I am the resurrection and life. He who believes in me will live even though he dies; and whoever lives and believes in me will never die.” Do you believe this?


Blessed are those who believe in Him. Amen!!!


Chichewa Version


Mawu Owerena: 1 Samuele 3:1-14, Luka 24: 13-24
Mutu: Mphamvu Ya Kuuka Kwa Ambuye Yesu Khristu Komanso Kuonekera Kwa Anthu Ake Okhulupilira


Tikhala tikulingalira kwambiri ku Chipangano chatsopano kumene tikumva nkhani ya anthu awiri; Kiliyopa ndi mnzake akukambilana pakati pa njira ulendo wa ku Emau koma tisanafike kumeneko tifuna tilingalire kwambiri nkhani yomwe yachokera ku chipangano chakale ku 1 Samuel 3:1-14
Tikumva nkhani ya kuitanidwa kwa Samuele. Samuele akuitanidwa ndi Mulungu ali m’nyumba ya wansembe, Eli. Samuele akuitanidwa katatu kufikira pamene tsopano Samuele akuyankha kuti “ine Ambuye ndili pano lankhulani.” Pa vesi 7 pali mau omwe akunena kuti “Panthawi imeneyi Samuele sanamudziwe Yehova ndipo mau a Yehova sanaululidwa kwa iye. Nthawi imeneyi Samuele amakhala nyumba ya Yehova, Amakakhala malo amene pamasungidwa likasa la Yehova koma Samuele sanamudziwe Yehova ndipo Mau a Yehova sanaulilidwa kwa iye. Tsoka ndilo nthawi imeneyo m’malo moyankha Yehova amathamangira kukayankha kw Eli. “Ndili pano pakuti mwandiitana.” Samuele amathamangira kwa munthu amene sakumuitana, yemwe analibe mphamvu pa kuitanidwa kwake.


M'chipangano chatsopano tawerenga Luka 24: 13-24 pomwe tikufuna kutsatira zochitika pa njira ya ku Emau. Yesu Khristu wauka kwa akufa. Akaudzionetsera kwa ophuznira ake, kwa omwe amamutsatira. Akudzionetsera kwa anthu omwe amamutsatira iye ndipo ena mwa iwo ndi anthu awiri amenewa. Anthuwa akuyenda ulendo wa ku Emau akukambirana za zimene zinachitika mu nthawi imene Yesu amazunzika, kupachikidwa, kuikidwa m’manda. Mu nthawi yomwe Yesu wauka kumanda chilichonse chomwe chachitika anthuwa akuyenda kumakambirana pa msewu.



Koma nkhani yomwe tikuikambirana ndi kupezeka kwa Yesu. Akuyenda mkumakamabirana za Yesu ndi pamenenso Yesuyo akufika pakati pawo ndi kumayenda naye limodzi. Yesu akufunsa kuti kodi zomwe mukukambiranazi ndiye ziti? Anthu aja akumuuza zomwe zinachitikazi kumamufunsanso kuti kodi inu simukudziwa kuti mneneri wathu amene timamdalira kuti adzabwera nadzatipulumutsa, nadzatipatsa moyo adzabwera, napachikidwa, naikidwa m’manda ndipo amayi ena anathamanga kupita kumeneko kukayang’ana m’manda ndipo apeza kuti kulibe? Anafotokoza momveka bwino kumuuza nkhani imeneyi mwini wakeyo, anthu awiriwa asakudziwa kuti mwini wake wa nkhani imeneyi ndi Yesu ameneyu.


Zoti Yesu wauka kumanda amadziwa koma zoti uyo amayankhula naye anali Iyeyu samadziwa. Tikunena za anthu amene ankamutsatira Yesu anakali ndi moyo, anthu amene ankakhala pafupi ndi Yesu adakali ndi moyo. Wauka tsopano kwa aakufa koma zoti waukazo sakudziwanso ayi, zoti munthuyo anali akuyenda naye pakati pawo njira yonse samazidziwa ayi.


Kuuka kwa Yesu Khristu, mphamvu ya kuuka kwa ambuye komanso kudzionetsera kwake kwa athu okhulupira
Tikufuna lero tione Yesu anauka chifukwa chiyani. Pali mphamvu yanji pa kuuka kwa ambuye pa moyo wa inu ndi ine? Yesu sanangouka ayi. Choyambirira anaukira anthu amene iwo akumudziwa Yesuyo kwambiri, akuyenda ndi iye kuti atsimikize za zonse zomwe amanena iye. Tamuona Samuele kuti iyeyu amakhala m’nyumba ya Yehova n’chifukwa chake tikunena kuti mphamvu iyiyi ikuyambira pakati pa okhulupilira enieniwo. Zitha kutheka n’kudzitcha okhulupilira koma osamudziwa Yesu. Zitha kutheka kukhala mkhirisitu zaka fote, migonero yonse ija kumadya, kumaima pano n’kumalalikira anthu mkumamva koma osamudziwa. Zoti malamulo khumi aja tinawaloweza n’kuwatsatira n’kumasunga pansi pa mtima koma Yesu osamudziwa. Samuele ankagona likasa lili kumutu kwake koma Yehova osamudziwa. Yesu anayenera kuuka kumanda kuti anthu awa akayambe kumudziwa tsopano. Abale awa awiriwa akunena kuti maso awo anagwidwa. Pofuna kutambasula Chichewa chotere kuti maso awo anagwidwa ndekuti nso amene anali nawo owonera m’mene timaoneramu anali osakwanira kumudziwira Yesu kufikira maso a mkati mwa mtima wa munthu atasegukabe.


Pa Aefeso 1:18 -19 amanena kuti kufikira maso a m’kati mwa mtima wathu atawalitsidwa pamenepo tikadziwa za chikondi chake, tikamudziwa Yesu wa kuuka kwa aakufa. Maso amene amafunika si awa anthu amayenderawa, maso ake si awa anthu akumayang’anira. Amafuna maso a m’kati mwa miyoyo yathu atseguke. Mwanjira ina, maso auzimu atseguke, kuuka kwa mwana wa Mulungu amene ali Yesu, ali ndi mphanvu yotsegula maso auzimu. Kuti maso athu azindikire choona chenicheni cha dziko lapansi ndi pokhapokha mzimu woyera atalowa pansi pa miyoyo yathu.


Tamverani nkhani ya abambo amenewa. Atafika kuti asiyane naye Yesu, anawakakamira kuti apite naye kunyumba kwawo. Sadamusiye kuti apite, kaya kungomuthokoza kuti Ambuye zikomo kwambiri. Anapita naye kunyumba kwawo kufikira atakhala naye pagome limene amanyema mkate nadya nawo limodzi, pamenepo maso awo anatseguka, anachanganuka, anawona ndipo anazindikira kuti uyu ndiye Mulungu, Yesu Khristu amene anaikidwa m’manda. Zikutengera inu ndi ine kuti tikhale naye Yesu Khristu m’kati mwa mitima yathu. Yesu ndiye Khristu tizamudziwa. Chifukwa mu Kuuka kwa Yesu muli mphamvu yakutsegula maso athu kuti timudziwe Yesu.



Yesu Cholinga chake amafuna titsegule, tidziwe Yesu amene timpembedza. Okondedwa m’mawa uno pa Machitidwe a Atumwi 9:18 Paulo ali m’kati mwa ntchito zake za ku midima kukapha aKhristu okhulupirira ku Damasiko. Atakumana ndi Yesu, akuti m’maso ake munatuluka zinthu zomwe zinakhala ngati mamba a nsomba zimene zinadzadza maso ake ndipo kuyambira pamenepo maso ake anatseguka atazindikira kuti wakumana ndi Yesu Kristu. Okondedwa maso amene tikuyendera lero pokhapokha tikumane ndi Yesu kuti titsegue tiwone ndekuti tidzamutumikira Yesu mu uzimu ndi mu choonadi.


Kuyenda ndi Yesu koma osamudziwa, kulankhula kumalankhula za Yesu koma osamudziwa, kumapembedza koma osamudziwa Yesu ndipo sizodabwitsa kuona kuti anthu amene timawadalira kunena kuti inu ndi amene mungatiuze za ukulu wake wa Yesu Khristu ndi amene amatikhumudwitsa kwambiri. Anthu amene akubwezeretsa dzina la Yehova kuti dziko lapansi lisapite patali m’mau a Yehova, abusa amene timawakhulupilira ndi amene amapitanso patsogolo ndi ntchito zawo zobwezeretsa m’mbuyo mau a Yehova. Maso auzimu agwidwa. Maso awo ndi akufa ndithu. Sakupenya. Sakudziwa. Mukumuona mkhristu akuledzera, ali dzandidzandi akuledzera nasautsika m’maso mwake ndi motseka. Yesu akutiyankhula kuti timukakamire Yesu ameneyu kut iyeyu mpaka akafike m’kati mwa moyo wake, muja anachitira Kaliyopa ndi mnzake, sanamusiye. Lero ndi tsiku lina labwino kuti Yesu atauka kwa akufa, Yesu atadziwonetsera pakati pathu, asapitilire m’banja mwathu asanapondemo, asapitilire mu mpingo mwathumu asanapondemo. Zitha kutheka kumayenda mumsewumu mpingo wa Zomba CCAP osapezekapo. Zitha kutheka Yesu wauka kwa akufa kumayenda m’nyumba za aneba athu koma m’banja mwathu osalowamo. Ndewu zokhazokha kungachere. Yesu anauka kwa akufa. Yesu atauka pakati pathu Yesu akukulamulirani penapake ndipo tikuyenera tidziwe kuti kuuka kwake akufuna timuzindikire tonsefe kuti tidziwe kuti waukadi kwa akufa mpulumutsi amene ife timulambira tikukondwera naye.


Nditsirize ndi mau awa. Maso a m’mitima yanu awalitsidwe kuti mukadziwa chiyembekezo cha kuitana kwa Yesu. Okondedwa, chuma cha ulemerero wa utumiki wathu chipezeka mwa yesu. Mphamvu yake ya kuuka kwa akufa ikhale pa ife lero ndi kunthawi za nthawi zonse mu dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, Amen

About Us

Zomba CCAP congregation, located in Zomba City, the old capital of Malawi, was established in 1898, and currently boasts 1,638 Christians, of which 115 are church elders and 103 church deacons. It has vibrant women and youth ministries, and a management team that co-ordinates the work of eleven committees, among which are the partnership, evangelism and intercessory, and music committee, as well as faith and works committee... Read more

Announcements & Events

Explosion 2023 Posted: 13 Apr, 2023
Zomba CCAP Holy Week Time Table Posted: 3 Apr, 2023

Address

Zomba C.C.A.P.
Chimbiya Road
P.O. Box 355, Zomba
+265 995 089 475

Newsletter