Sermons

M’moyo Wa Chikhristu Timakumana Ndi Zofowoka Zambiri

      

Mawu Oyamba


Mabuku onse a Uthenga wabwino akutsimikiza za kuwuka kwa Ambuye Yesu. Yohane akufotokoza za kuonekera kwa ophunzira ake katatu. Marko akunena kuti anaonekera kanayi koma kwa ophunzira anaonekera katatu. Akutipatsa phunziro kuti ophunzira a Yesi anali osakhazikika kwenikweni Yesu asanakwere kumwamba. Anali ndi chifowoko.


Kutambasula Mawu


Mu thupi lathu ndikovuta kutumikira moona. Popanda mzimu woyera sitingathe kutumikira. Pamene ophunzira anali kukambirana za kuonekera kwa Yesu, Thomasi panalibepo, koma Yesu anali mu thupi la uzimu ndipo sanamuona. Anabwera ulendo wina pamene Thomasi analipo ndipo anamuuza kuti amukhudze. Ndipo Thomas anakhulupirira nagwada pansi mogonja. Ndipo Yesu anawachokera.


Nthawi yomweyo Petro anakonza zokapha nsomba kusiya ntchito imene Yesu anawasiyira. Yohane sakulemba za ntchito imene ophunzira ankachita koma akukamba zomwe ananena Yohane mbatizi kuti anawalozera ophunzira ake kwa Yesu amene anayenera kumutsatira osati iye Yohane Mbatizi. Apa akufuna kutisonyeza kuti ophunzirawa anali asodzi ndipo anabwereranso ku usodzi wawo. M’moyo wathu timateronso. Nyengo zikavuta timabwereranso pansi. Ngati nyengo zimenezi sitisamala nazo timatha kupwetekeka. Tiyenera kukhala osamala. Koma tikuona kuti pamene Petro ndi anzake akubwerera ku usodzi sizikuwayendera ngakhale poyamba anali akatswiri pa ntchitoyi.


Atapita kopha nsomba sanagwire kanthu. Tikamusiya Mulungu sitingachite bwino. Zikamayenda amakhala Mulungu. Mulungu amafuna kutiumba kuti timutumikire bwino ngakhale kuntchito kwathu. Tikakhala pa udindo titumikirenso Mulungu. Petro ndi anzake sanaphe chilichonse. Yesu anadziwa kuti iwo anagalukira. (Yesu anati Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine). Yesu anabwera pamene panali Petro ndi anzake modzizimbayitsa ndipo iwo sanamuzindikire. Anawafunsa ngati anagwirako nsomba. Iwo anati ‘ayi.’ Anawauza kuti aponye kudzanja lamanja la boti. Ataponya anagwira nsomba 1800 zazikulu koma khoka silinang’ambike. Petro anamuzindikira Yesu ndipo anavala zovala popeza anali maliseche pamene anali kupha nsomba. Petro anamva chisoni popeza analonjeza kukhala ndi ambuye nthawi zonse. Koma anamuthawa. Tikuyenera kumadzifunsa za moyo wathu pa chikhulupiriro chathu pa Mulungu. Ndi chiyani chimatilepheretsa kukhala okhulupirira. Petro anafika pamenepa ndipo ananena mawu; “Ambuye chokani kwa ine chifukwa ndine osaenera.” Sanalabade za nsomba zomwe anapha zija. Anasokeretsa anzake. Mwina ifenso tachita zimenezo. Yesu analibe nazo ntchito. Petro ananena kuti sachita manyazi kukhulupirira Yesu. Ifenso moyo wathu uzifika pamenepa, kugonja pamene tachimwa. Timapeza chilimbikitso. Yesu anawauza kuti atenge nsomba aotche nadya limodzi kuwalimbikitsa kuti anaukadi ndipo anali pakati pawo. Yesu ali pamwamba ndipo chilichonse ndi chotheka ndi iye. Palibe chomwe chingatisiyanitse ndi chikondi chake. Iyeyo ndi amene amalimbana ndi Satana.
Maphunziro



  1. Popanda Yesu sitingapeze chigonjetso. Ophunzira anayesera usiku onse koma analephera. Mulungu amatidziwa. Mulungu akavomera mapulani athu amayenda. Pamene Yesu wauka akutiphunzitsa kuti sitingathe kuchita zilizonse popanda Yesu. Timulandire ngati mbuye ndi mphulumutsi wathu.

  2. Yesu ndi zonse mu zonse. Petro anakasodza usiku nalephera kupha nsomba koma Yesu anawapeza usana ndipo anawauza kuti aponye khokha ndipo anapha nsomba. Tiyeni timumvere Yesu. Akuti ‘khulupirirani ine, idzani kuno onse olema ndi othodwa.’ Yesu alibe nyengo, ndi zonse mu zonse. Tisavutike Yesu alipo amene ali yankho la mavuto athu onse. Ambuye akutiitana kuti timumvere.

  3. Yesu amapereka chilichonse. Ophunzira aja analibe chakudya koma Yesu anawapezetsa chakudya. Nthawi zina timakakamira zinthu koma sitidzapita nazo monga Yobu akunena ‘ndinabwera opanda kanthu ndidzapitanso opanda kanthu.’ Ophunzira anathawa Yesu koma anawatsatira nawapatsa chakudya. Popanda Yesu sitingapeze chilichonse. Moyo wathu mwini wake ndi Yesu. Yesu amatikonda monga anasonyezera pamtanda paja. Ife sitikanatha kulimbana ndi satana ndi kudziombola. Tikufunikira Mphamvu ya Yesu kuti tiyende mu chilungamo. Ambuye ativeke ulemerero watsopano moyo wosachimwachimwa, atithandize kuzindikira kuti Madalitso amene tili nawo ndi a Mulungu ndipo tiwagwiritse bwino ntchito.

About Us

Zomba CCAP congregation, located in Zomba City, the old capital of Malawi, was established in 1898, and currently boasts 1,638 Christians, of which 115 are church elders and 103 church deacons. It has vibrant women and youth ministries, and a management team that co-ordinates the work of eleven committees, among which are the partnership, evangelism and intercessory, and music committee, as well as faith and works committee... Read more

Announcements & Events

Explosion 2023 Posted: 13 Apr, 2023
Zomba CCAP Holy Week Time Table Posted: 3 Apr, 2023

Address

Zomba C.C.A.P.
Chimbiya Road
P.O. Box 355, Zomba
+265 995 089 475

Newsletter