Sermons

Koma Si Monga Mwakufuna Kwanga Koma Chifuniro Chanu Ndithu

      

Mawu Owerengedwa: Yesaya 53:1-7, Ahebri 10:32-36, Mateyu 26:36-50


Mawu Oyamba


“Ambuye ngati mufuna chikho ichi chindipitirire. Koma si monga mwakufuna kwanga koma chifuniro chanu ndithu.” Yesaya 53
akufotokoza molunjika za kubwera kwa Ambuye Yesu ndi za mazunzo ake. Zimenezi sizinangochitika ayi, zinali zitanenedwa kale ku chipangano chakale kotero sitikuyenera kukayika konse za mawu a Mulungu.


Kutambasula Mawu


Paulo kwa Afilipi akulimbikitsa kuti apilire ndithu kuti akalandire mphoto.
Ku Mateyu mkangano wa pakati pa mdima ndi kuwala wafika pachimake.
Zimene zikuchitika mu m’munda wa Getsemane ndi chiyindeyinde. Cholinga cha kubadwa kwa Yesu ndi kudzapulumutsa anthu ake ku machimo. Ambuye Yesu anakumbukira cholinga chimenechi. M’moyo wake wonse anali ndi adani kuyambira pa kubadwa kwake pamene anazondedwa ndi mfumu Herode mpaka m’munda wa Getsemane. Anamuchotsa m’kachisi pa ulaliki wake woyamba. Anthu anamuda ngakhale anawachitira zabwino monga kuchiza odwala, kuwukitsa akufa komanso kuwadyetsa. Ambuye Yesu sanabise uthenga ngakhale zonsezi zinamuchitikira.


Yesu anawafunsa akulu ansembe kuti iye ndani. Iwo anati ndi mwana wa Davide. Koma iye anafunsa kuti nanga ndi chifukwa chiyani Davide ananena za Yesu ngati Mbuye wanga. Iwo anakwiya naye. Anamuchitira upo womupha. Ophunzira m’munda wa Getsemane anamva kuchoka kwa Yesu akunena zomwe m’mbuyomu sanaziyankhule. Moyo unafika powawa, ponzunzika. Yesu anagwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru. Anali akudziwa zomwe zinali kuchitika m’masiku otsatira. Anaiona imfa. Anapemphera kuti chikho chimupitirire koma osati mwakufuna kwake. Anazindikira za cholinga chake chodzapulumutsa anthu. Anafuna kupempha njira ina. Ifenso timafika mu ndime zowawa, kusala, kupemphera koma nyengo osasintha. Koma Yesu akuti chifuniro chanu chichitike.


Maphunziro



  1. Moyo uno utumiki wathu umatifikitsa pena pozingwa. Timadutsa mu nyengo zowawa. Koma tisadzidzimuke konse chifukwa ndiye moyowo. Timafika pofuna kutaya utumiki. Ndipo zovuta siziona kuti uyu ndani. Ngakhale mbusa ndi okhulupirira ena onse amakhudzidwa ndithu ndi zovuta. Koma uthenga ndi wakuti “Pilirani kuti mukalandire mdalitso”.

  2. Mukaonana ndi ena ozingwa tenganipo gawo. Ambuye anatenga ophunzira mu Getsemane. Anawauza ‘pempherani nane limodzi’. Tikhale achilimbikitso kwa ena.

  3. Ambuye Yesu akuti ‘ngati mukufuna chindipitirire koma sikufuna kwanga.’ Yesu ndi Ambuye ndipo tayenera kugonjera ku chifuniro chake. Gonjerani ku chifuniro chake, osapanga chiganizo chotsutsana ndi Ambuye. Ambuye anali okhulupirika kufikira imfa yake pamtanda. Yesu anadziwiratu za mazunzo ake pamtanda koma anagonjera chifuniro cha Mulungu. Tiyike maso athu patsogolo.

  4. Ngati anthu angazunzike asazunzike chifukwa cha inu. Ambuye Yesu anazunzika ndi afalisi. Mdiyerekezi asakwaniritse zolinga zake kudzera mwa ife.

  5. Pa zopweteka zonse Ambuye Yesu anasankha kupemphera. Anapemphera zolimba. Moyo ukawawa tipemphere. Tiye tiziswera m’mabwalo a Ambuye. Pamene nkhondo, ikubwera tipemphere.

About Us

Zomba CCAP congregation, located in Zomba City, the old capital of Malawi, was established in 1898, and currently boasts 1,638 Christians, of which 115 are church elders and 103 church deacons. It has vibrant women and youth ministries, and a management team that co-ordinates the work of eleven committees, among which are the partnership, evangelism and intercessory, and music committee, as well as faith and works committee... Read more

Announcements & Events

Explosion 2023 Posted: 13 Apr, 2023
Zomba CCAP Holy Week Time Table Posted: 3 Apr, 2023

Address

Zomba C.C.A.P.
Chimbiya Road
P.O. Box 355, Zomba
+265 995 089 475

Newsletter