Kupereka Mokondwera
Kupereka anayamba ndi Mulungu monga tiwerengera pa Yohane 3:16 pamene Mulungu anapereka mwana wake wobadwa yekha ku dziko lonse kuti dziko lipeze chipulumutso.
Ichi ndi chitsanzo chabwino chifukwa Mulungu akupereka mosawinya, mwana wake yekhayo wokondedwa, Yesu Khristu. Choncho Mulungu ndiye chitsanzo chathu.
Kupereka mokondwera ndi machitidwe amene amachitika kuchokera mu mtima wokondwera n...